CHIWERENGERO CHA ANTHU OMWE AONETSA CHIDWI CHODZAPIKISANA PAMPANDO WA UTSOGOLERI WADZIKO CHAFIKA PA 13.

Mtsogoleri wa chipani cha People’s Transformation (Petra) a Kamuzu Walter Chiwambo komanso a Smart Swira omwe ndioima paokha, lero atenga kalata zosonyeza chidwi chodzapikisana nawo pa mpando wa utsogoleri wadziko lino pa chisankho chomwe chichitike mwezi wa September.

Malinga ndi mkulu ofalitsa nkhani ku bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) a Sangwani Mwafulirwa, atsimikizira izi URS Online lero lachisanu pambuyo potsendera kupereka kalatazi kwasabata ino.

Izi zikutathauza kuti omwe atenga kalatazi tsopano akwana khumi ndi atatu (13).

Ena mwatsogoleri omwe atenga kale kalatazi ndi a Milward Tobias, oima paokha, a Adil James Chilungo, oima paokha, a Lazarus McCarthy Chakwera achipani cholamula cha Malawi Congress (MCP), a Kondwani Nankhumwa, achipani cha Peoples Development (PDP), a Akwame Bandawe,l, achipani cha Anyamata, Atsikana, Azimayi (AAA), a Joyce Banda, achipani cha People’s (PP), a Atupele Austin Muluzi, achipani cha United Democratic Front (UDF), a Reverend Hardwick Kaliya, oima paokha, a Arthur Peter Mutharika, achipani cha Democratic Progressive (DPP), a Frank Tumpale Mwenifumbo, achipani cha National Development (NDP) ndi a Dalitso Kababmbe, achipani cha UTM.

Related posts

MCP TO HOLD A PRESS BRIEFING AIMED TO SHARPENING THE PARTY’S FUTURE.

MKULU WINA WAPHA BAMBO AKE KAAMBA KAMPUNGA.

BOMA LAPEREKA NDALAMA ZOPOSERA K7 MILLION KUTI ZITHANDIZIRE MWAMBO WAMALIRO KWA MZIKA ZOMWE ZINAFA PANGOZI YA BUS.