UMOYOSPORTS

UmoyoSports

Bungwe la Superleague Of Malawi Sulom,latulutsa mndandanda wa mmene masewero akhalire mu sabata Yoyamba mu Ligi yaikulu ya mdziko muno ya FDH Bank Premiership.

Mwa zina pa mndandanda wo pakuonetsa kuti Bwalo la Kamuzu lomwe Bungwe la Football Association Of Malawi Fam,linalengetsa kuti sinafikire mulingo okuti mkuchititsa masewero a mipikisano ikulu ikulu ya mdziko muno ili pa mndandanda ozachititsa masewero otsekulira Ligi a pakati pa Mighty Wanderers komanso Karonga United loweruka pa 25 April 2026

Mndandanda onse mu sabata Yoyamba ukuoneka Motere :

Loweruka pa 25 April 2026

  • Mighty Wanderers vs Karonga United @Kamuzu
  • Moyale Barracks vs Goshen City Dedza Dynamos @Rumphi
  • Civil Service United vs FCB Nyasa Big Bullets @Civo
  • Kamuzu Barracks vs Silver Strikers @Champions

Lamulungu pa 26th April 2026

  • Masters FC vs Chitipa United @Bingu
  • Blue Eagles FC vs Ekhaya FC @Civo
  • Red Lions vs Creck Sporting Club @Zomba
  • Mafco FC vs Mitundu Baptist @Champions.

Wolemba: Williams Chande (21/04/2026)

umoyofm107.8Mhz

LiwulaUmoyoKwaAliyense

Related posts

ya ulimi

ANTHU OFUNA THANDIZO LA CHITUPA CHOTUKUKIRA MDZIKO ASIMBA LOKOMA.