
Dalaivala wina alimmanja mwa apolisi ataomba ndikupha ana awiri m’mudzi mwa Sumaili m’boma la Mangochi.
Sharifu Duwa wazaka 10 ndi Kifa Charles wazaka 9 anaombedwa pomwe amaoloka msewu ndi galimoto la mtundu wa Toyota Sienta lomwe limayendetsedwa ndi a Shafi Kassim azaka 28, lolemba pa 11 May 2026, omwe anathawa kusiya galimoto pamalopo zitachitika izi.
Malingana ndi ofalitsa nkhani zapolisi m’bomali Inspector Amina Tepan Daud wati anawo anavulala kwambiri mmutu komanso kuthyoka mafupa amiyendo yakumanzere ndipo anamwalilira munjira pomwe amathamangira nawo ku chipatala cha Namwera Health Centre kuti akalandire thandizo.
A Daud ati m’mawa wa lachiwiri pa 12 May 2026 a Kassim akazipereka okha kupolisi, ndipo akuyembekezereka kuyankha milandu yokupha poyendetsa galimoto mosasamala komanso pokanika kuthandiza anawo powapititsa kuchipatala atagundidwa.
Omwalirawa onse amachokera m’mudzi mwa Salimu mfumu yaikulu Jalasi m’boma lomweli la Mangochi.