
Boma lalamula ofesi ya mnthambi yopanga zitupa zolowera ndi kutulukira mdziko yamumzinda wa Blantyre (Immigration) kuti mwezi uno ukamatha ikhale yatulutsa mlingo wazitupa zosachepera theka la anthu omwe anapereka kale ndalama.
A Norman Chisale omwe ndi wachiwiri kwanduna yoona zachitetezo chamdziko anena izi lero pomwe anayendera ofesi zamnthambiyi.
A Chisale ati mtsogoleri wadziko lino Professor Arthur Peter Mutharika ndi yemwe walamula pofuna kuonetsetsa kuti m’Malawi aliyense yemwe akufuna thandizo la chitupali athandizidwe munthawi yake.
Ndunayi yachenjeza ogwira ntchito kumnthambizi apewe mchitidwe wakatangale maka olandira ndalama zoonjezera panthawi yomwe anthu akufuna thandizoli.
Pakalipano iwo apereka mphamvu kwa anthu ofuna chitupachi kufika kuofesi yawo nthawi iliyonse ngati ogwira ntchito alowetsapo zakatangale Kuti awaneneze.