
Bambo wina White Mussa wazaka 26 ku Mangochi akuyembekezereka kuyankha mlandu kaamba kopha bambo ake atasemphana maganizo pathumba la mpunga zomwe ndizosemphana ndi gawo 209 loyendetsera malamulo adziko lino.
Ofalitsa nkhani zapolisi m’bomali Inspector Amina Tepan Daud wati izi zachitika usiku wadzulo lachiwiri pa 12 May m’mudzi mwa Maluwa 2 mfumu yaikulu Chowe.
Daud wati malemuwo a George Mussa Mkumba patsikuli anakaniza mwana wawoyo kutenga thumba la mpunga lomwe iye amafuna kutengera mphamvu pomwe amabwelera kwa mkazi wake yemwe anasemphana nae zachitika.Mkangano utakula oganiziridwayu anamenya pamutu bambo akewo ndi chimtengo omwe anakomokeratu pompo ndipo anatera muJira pofika nawo ku chipatala chachikulu cha Mangochi.
White Mussa amachokera m’mudzi mwa Bamusi mfumu yaikulu Chiunda m’boma lomweli la Mangochi.