LERO KUOMBA MPHEPO YOTHAMANGA MAKILOMITA 36 PAOLA ILIYONSE YATERO NTHAMBI YA ZANYENGO.

Mnthambi yoona zanyengo ndikusintha kwa nyengo (Department of Climate Change and Meteorological Services) yamema anthu okhala m’madera amphepete mwanyanja kuti akhale tcheru ndi mphepo yamphamvu ya Mwera yomwe iombe kuyambira lero lachinayi pa 3 April mpaka lamulungu pa 6.

Izi zili chomwechi malinga ndi akatswiri kumnthambiyi omwe ati mphepoyi ikuyembezeleka kuomba pamtunda othamangira makilomita 36 paola iliyonse komanso kuchititsa mafunde odzetsa mankhalu otalika lipande limodzi (1 metre) .

Iwo apempha anthu omwe amagwiritsa ntchito nyanjayi kukhala osamala kuopa kutaya miyoyo yawo ndi katundu.

Ndipo mawa lachisanu, akatswiriwa akudziwitsanso anthu okhala m’madera amphepete mwanyanja ya Malawi kuti kudzaomba chimphepo chomwe chidzasakanikilane ndi mvula yamphamvu yomwe idzapangitse madzi kusefukira.

Chidziwitso : makina alipachithunzipo ndiomwe amathandizira mnthambiyi kupima mlingo wamphepo komanso kusefukira kwamadzi

Related posts

MCP TO HOLD A PRESS BRIEFING AIMED TO SHARPENING THE PARTY’S FUTURE.

MKULU WINA WAPHA BAMBO AKE KAAMBA KAMPUNGA.

BOMA LAPEREKA NDALAMA ZOPOSERA K7 MILLION KUTI ZITHANDIZIRE MWAMBO WAMALIRO KWA MZIKA ZOMWE ZINAFA PANGOZI YA BUS.