Home Uncategorized NJOBVU YOLUSA YAPHA MLIMI WINA KU MANGOCHI.

NJOBVU YOLUSA YAPHA MLIMI WINA KU MANGOCHI.

by Mclove Mafuta
0 comments

Mlimi wina waphedwa ndi njobvu yolusa kufupi ndi nkhalango ya Namizimu m’boma la Mangochi.

Ofalitsa nkhani zapolisi m’bomali Inspector Amina Tepani Daudi, watsikimizira URS kuti mlimiyo ndi a Shaibu Bunanji azaka 50 ndipo lamulungu pa 29 March anakumana ndi njobvuyo pomwe amakathamangitsa anyani omwe amamuonongera mbeu zawo.

Malingana ndi Daudi, ati anthu ozungulira omwe amaona izi zikuchitika anayetsetsa kuthamangitsa chilombocho koma zinakanika mpaka chinakwanitsa kuvulaza a Bunanji mpaka kufa.

Pakadali pano, apolisi atengera nkhaniyi ku nthambi yowona za nyama zakutchire kuti achitepo kanthu.

A Bunanji amachokera m’mudzi mwa Chapola, m’dera la mfumu yayikulu Chowe ku Mangochi.

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00