


Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera lero watsegulira ofesi zatsopano zakhonsolo ya boma la Thyolo yomwe yadya ndalama zokwana K7.9m.
Ofesizi zomwe ndizoposa makumi asanu ndiziwiri (70) mukhale mnthambi zonse zaboma zilipansi pakhonsoloyi komwe anthu azitha kupeza thandizo posatha mtunda.
M’mawu awo Dr Chakwera ati boma lawo silikuona mtundu, chikhalidwe, chipembezo kapena dera koma iwo akuthandiza mzika iliyonse yokhala mdziko muno.
Pomaliza Dr Chakwera apempha anthu kukhala ololerana komanso ogwirizana pochita zinthu kuti chitukuko chadziko lino chizimka napita patsogolo.
Pakalipano mtsogoleri wadziko linoyu akuyembekezeleka kukatseguliranso bwalo la zamasewero latsopano m’boma la Zomba.