Home Uncategorized AMAI OMWE AKUPIKISANA M’MIPANDO YOSIYANASIYANA PACHISANKHO CHAPA 16 KU MANGOCHI AWAPATSA UKADAULO WAPADERADERA OKOPERA ANTHU.

AMAI OMWE AKUPIKISANA M’MIPANDO YOSIYANASIYANA PACHISANKHO CHAPA 16 KU MANGOCHI AWAPATSA UKADAULO WAPADERADERA OKOPERA ANTHU.

by Mclove Mafuta
0 comments

Namatetule pandale mai Patricia Kaliati apempha amai omwe akupikisana mipando yosiyanasiyana pachisankho chapa 16 September kuti alunjike pamfundo zawo zachitukuko panthawi yomwe akuchititsa misonkhano yawo yokopa anthu.

A Kaliati omwe anali mlendo olemekezeka apereka pempholi ku Mangochi, pamkumano omwe unakonzedwa ndi bungwe lolimbikitsa amai kupikisana nawo pa ndale la Centre of Civic Society Strengthening.

Iwo ati kudzikweza panthawi yomwe akuchita misonkhano yawo kutha kuchepetsa mwai wawo opambana kotero nthawi isanathe akuyenera kukhala odekha ndipo atambasule zitukuko zomwe azawachitire anthu akudera kwawo.

“Sichinthu chabwino kuima pamsonkhano mkumalengeza kuti ife ndi owinawina!uko amayi amzanga dziwani kuti ndikulakwitsa chifukwa voti ya munthu imafunika kunyengelera polunjika pazomwe iye akufuna”. Anatero a Kaliati.

Potsiridza a Kaliati amemanso amayiwa kuti achilimike kunyengo zomwe angakumane nazo monga kulandira zitonzo zosiyanasiyana kuchokera kwa abambo omwe akupikisana nawo zomwe zingawafooketse kuti asiyire panjira ndipo atsindika ponena kuti nthawi yakwana yoti amai ochuluka alowe m’bwalo.

Pothilirapo ndemanga a Flora Habibu Paseli, oima paokha omwe akupikisana nawo pa mpando wa ukhansala mu ward ya Majuni m’boma la Mangochi, ati aphunzira zambiri kudzera kumkumanowu monga kulimba mtima, posaziyang’anira pansi kuphatikizirapo ukadaulo wamene angakopele anthu kuti awavotere.

A Paseli atinso maphunzirowa mwazina awasintha kaganizidwe kochita ndale zawo monyoza ena kuti akondedwe koma kutsamira mfundo zomwe zingathetse mavuto lomwe dera lawo lilinawo mothandizidwa ndi khonsolo, anthu akufuna kwabwino, abwenzi komanso thandizo la mipingo logwira ntchito zachifundo.

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00