Home Uncategorized CHAKWERA WAYAMIKIRA RBM PANTCHITO YABWINO YOMWE IKUGWIRA POBWEDZERETSA CHUMA MDZIKO MUNO.

CHAKWERA WAYAMIKIRA RBM PANTCHITO YABWINO YOMWE IKUGWIRA POBWEDZERETSA CHUMA MDZIKO MUNO.

by Mclove Mafuta
0 comments

Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCathy Chakwera wayamikira bank ya Reserve (RBM) kaamba kochilimika pochepetsa mavuto akusowa kwa ndalama zakunja.

Dr Chakwera ayankhula izi lero ku Lilongwe pamwambo okumbukira kuti bankiyi yatha zaka makumi asanu ndi limodzi (60) ikugwira ntchito zake, poonetsetsa kuti chuma chadziko lino chikuyenda bwino.

Iwo ayamikiranso bankiyi kaamba koika ndondomeko zina zamakono loti dziko lino lidzipata phindu lochuluka kudzera muntchito zake.

M’mawu awo Dr McDonald Mafuta Mwale omwe ndi mkulu wanankiyi, ati pofuna kuthana ndimavuto azachuma omwe dziko lino limakumana nawo, pakufunika kuchilimika maka pomatumiza ndikugulitsa katundu wapamwamba m’maiko akunja.

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00