Home Uncategorized KALATA ZOLIMBIRANA MPANDO WA UTSOGOLERI WADZIKO ZOKWANA 17 NDIZO ZATENGEDWA PAKADALIPANO.

KALATA ZOLIMBIRANA MPANDO WA UTSOGOLERI WADZIKO ZOKWANA 17 NDIZO ZATENGEDWA PAKADALIPANO.

by Mclove Mafuta
0 comments

Mpikisano otenga kalata zosonyeza chidwi chodzapikisana nawo pa mpando wa utsogoleri wadziko muchisankho chapa 16 September ukupitilirabe kukula pomwe lero kalata inanso yatengedwa.

Malingana ndi mkulu ofalitsa nkhani ku bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) a Sangwani Mwafulirwa atsindika ponena kuti lachisanu pa 11 July, a Dr Daniel Dube omwe ndi mtsogoleri wachipani cha National Patriotic (NPP) ndiomwe atenga kalatayi kufikitsa chiwerengero cha anthu olimbirana mpandowu kufika pa khumi ndi zisanu ndi ziwiri (17).

A Mwafulirwa ati ndandanda wa anthu onse omwe atenga kalatazi potsendera sabata ino uli motere:

A Milward Tobias, oima paokha, a Adil James Chilungo oima paokha, a Lazarus McCarthy Chakwera, achipani cha Malawi Congress (MCP), a Kondwani Nankhumwa achipani cha People’s Development (PDP), Akwame Bandawe achipani cha Anyamata, Atsikana, Azimayi (AAA), a Joyce Banda, achipani cha People’s (PP), Atupele Austin Muluzi, achipani cha United Democratic Front (UDF), a Reverend Hardwick Kaliya, oima paokha, Arthur Peter Mutharika, a Democratic Progressive (DPP), a Frank Tumpale Mwenifumbo, achipani cha National Development (NDP), a Dalitso Kabambe a chipani cha UTM, a Kamuzu Walter Chibambo, achipani cha People’s Transformation (Petra), a Smart Swira oima paokha, a David Mbewe, achipani cha Liberation for Economic Freedom (LEFP), a Cassim Chilumpha, achipani cha Assembly for Democracy and Development (ADD), a Cosmas Felix Chipojola, oima paokha ndi a Daniel Dube achipani cha National Patriotic (NPP).

Potsiriza a Mwafulirwa akumbutsa anthu onse kuti lolemba likudzali pa 14 July,2025 bungwe la MEC likhala ndi mwambo okhadzikitsa nyengo yopangitsa misonkhano yokopa anthu ndipo uchitikira ku BICC mumzinda wa Lilongwe.

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00