Home Uncategorized NTHAMBI YA ZANKHALANGO YALANDA MATUMBA AMAKALA OKWANA 212 OPANDA CHITUPA.

NTHAMBI YA ZANKHALANGO YALANDA MATUMBA AMAKALA OKWANA 212 OPANDA CHITUPA.

by Mclove Mafuta
0 comments

Bambo wina wazaka 31 ku Mangochi ali m’manja mwapolisi kaamba kopezeka ndimakala opanda chilolezo.

Malinga ndi mneneri wapolisi m’bomali Inspector Amina Tepan Daudi wati bamboyu yemwe dzina lake ndi Mark Yusuf ochokera m’mudzi mwa Chomba mfumu yaikulu Mponda m’boma lomweli la Mangochi anamunjata kum’mawa kwa lachitatu pa 30 April ntownship yabomali atatsinidwa khutu kuti mkuluyo akutsitsa matumba ankhaninkhani kunyumba kwake.

Poyankhula ndi Umoyo Radio Online a Daudi ati iwo limodzi ndi ofesi yoyang’anira nkhalango m’bomali atakachita chipikisheni kunyumbayo anakwanitsa kupeza matumba amakala okwana 212 komanso zipika zamitengo zokwana 27.

Yusuf akuyembekezeleka kukayankha mlandu ogwiritsa ntchito nkhalango opanda chilolezo.

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00