Home Uncategorized UNDUNA WAZA UMOYO WAPEMPHA ANTHU KUTENGA NAWO MBALI POKUMBUKIRA MATENDA A ULUMALI OZELEZEKA AMU UBONGO.

UNDUNA WAZA UMOYO WAPEMPHA ANTHU KUTENGA NAWO MBALI POKUMBUKIRA MATENDA A ULUMALI OZELEZEKA AMU UBONGO.

by Mclove Mafuta
0 comments

Unduna waza Umoyo mogwirizana ndi bungwe la Autism Hope Trust ndimabungwe ena wati pa 26 mwezi uno uchititsa mwambo okumbukira matenda aulumali ozelezeka mu ubongo.

Mlembi kundunawu Dr Samson Mndolo ndiomwe anena izi kudzera muchikalata chomwe undunawu watulutsa lachitatu pa 2 April.

Poyankhula ndi Umoyo Community Radio Station (UCRS) a Mndolo ati matendawa omwe padziko lonse amakumbukilidwa pa 2 April chaka chilichonse, kuno kumudzi tsikuli alikumbukira pa 26 pamutu oti “ubongo wamunthu aliyense ungathe kugwiritsidwa ntchito mosiyanasiyana pachitukuko chadziko lino” ndipo udzachitikira m’mizinda ya Mzuzu, Blantyre ndi Lilongwe.

Iwo ati mutuwu uthandizira kutsindika zakufunika kozindikira ndikuvomereza anthu omwe ali ndi ulumali ozelezeka wamu ubongo kuti ali ndigawo lalikulu pankhani yachitukuko chadziko komanso ufulu okhala momasuka pamodzi ndi anthu ena.

Kafukufuku waonetsa kuti mwana m’modzi mwa ana 100 aliwonse padziko lapansi amadwala nthenda ya ulumali ozelezeka mu
ubongo.

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00