
Gulu lotchedwa Mangochi-Makanjira Road Concerned Citizens lati lachiwiri pa 24 June, lichita zionetsero zofuna kukakamiza boma kuti likwaniritse lonjezano lake lomanga msewu wa Mangochi-Makanjira.
Izi zadza pambuyo pamkumano omwe gululi lachititsa lachisanu pa 20 June, ndi akuluakulu akhonsolo ya Mangochi motsogodzedwa ndi bwanamkubwa a Davie Chigwenembe, a Ernest Kadzokoya omwe ndi mkulu wamzinda wabomali ndinso apolisi.
Poyankhula ndi URS Online ofalitsa nkhani kugululi a Masauko Banda ati mkumanowu wayenda bwino ndipo atsindika kuti zionetserozi zomwe zidzayambire pa round-about ya Bakili Muluzi Highway, kuyambira 9 koloko m’mawa zidzakhala zabata ndi mtendere.