
Wachiwiri kwamtsogoleri wadziko lino Dr Michael Usi wafika mdziko la Mozambique komwe akakhale nawo pamwambo okumbukira tsiku lomwe dzikolo linalandira Ufulu odzilamulira omwe uchitike lachitatu pa 25 June pa stadium ya Machava mumzinda wa Maputo.
Pofika mdziko la Mozambique a Usi omwe akukaimilira mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCathy Chakwera alandilidwa ndi nduna yoona zamaubale amaiko ena a Maria Manuela Dos Santos Lucas komanso kazembe wadziko lino ku Mozambique a Wezi Moyo
Ulendowu boma lati uthandizira kukambirana komanso kulimbitsa ubale wamaiko awiriwa pankhani zamalonda.