Unduna waza Umoyo mogwirizana ndi bungwe la Autism Hope Trust ndimabungwe ena wati pa 26 mwezi uno uchititsa mwambo okumbukira matenda aulumali ozelezeka mu ubongo.
Mlembi kundunawu Dr Samson Mndolo ndiomwe anena izi kudzera muchikalata chomwe undunawu watulutsa lachitatu pa 2 April.
Poyankhula ndi Umoyo Community Radio Station (UCRS) a Mndolo ati matendawa omwe padziko lonse amakumbukilidwa pa 2 April chaka chilichonse, kuno kumudzi tsikuli alikumbukira pa 26 pamutu oti “ubongo wamunthu aliyense ungathe kugwiritsidwa ntchito mosiyanasiyana pachitukuko chadziko lino” ndipo udzachitikira m’mizinda ya Mzuzu, Blantyre ndi Lilongwe.
Iwo ati mutuwu uthandizira kutsindika zakufunika kozindikira ndikuvomereza anthu omwe ali ndi ulumali ozelezeka wamu ubongo kuti ali ndigawo lalikulu pankhani yachitukuko chadziko komanso ufulu okhala momasuka pamodzi ndi anthu ena.
Kafukufuku waonetsa kuti mwana m’modzi mwa ana 100 aliwonse padziko lapansi amadwala nthenda ya ulumali ozelezeka mu
ubongo.