Home Uncategorized TIKUYEMBEKEZERA MASEWELO APAMWAMBA

TIKUYEMBEKEZERA MASEWELO APAMWAMBA

by Mclove Mafuta
0 comments

Bungwe la Eastern Region Football Association linakonza nkumano ndi Eni ma timu omwe akutumikira mu chikho cha Durata Priemer Division komanso division one ndi cholinga chowunika momwe mpikisanowu wandera mu gawo loyamba.

Mtsogoleri wa bungweli a Issah Ibrahim anati nkumanowu wathandizira kuwunikirana zotsamwitsa komanso za bwino akumana nazo mu gawoli ndipo ali ndi chikhulupiriro kuti mu gawo la chiwiri ukhale mpikisano wa pa mwamba kwambiri.

A Matthews Kanteza yemwe ndi M’phunzitsi wa timu ya Prison United anati nkumanowu unali ofunikira kwambiri, chifukwa wathandizira kuti atule nkhawa zawo.

Mwa dzina Kanteza adati kagwiridwe ka ntchito ka oyimbira mpira pena akamapanga ziganizo dzina zikumakhala zolakwika .

Pothilira ndemanga, mtsogoleri oyang’anira oyimbira mpira mchigawo cha ku M’mawa a Henry Bello adavomereza za mavuto ena omwe amakhala akuchiti mma bwalo ena pakati pa oyimbira komanso Ma timu.

Kotero, a Bello adati akonza vutoli ndi cholinga choti masewero a mu gawo la chiwiri pasakhale zotsamwitsa.

Masewero okwana 74 ndi amene aseweredwe m’gawo la chiwiri mu chikho cha Durata Priemer Division komanso division one. Ndipo ayamba pa 12 October 2025.

Wolemba Iqra Adani

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00