Anthu a m’mudzi mwa Saiti Mwasungu, T/A Makanjira m’boma la Mangochi akukumana ndi mavuto kamba ka ntchito za migodi zomwe zikuchitika mderali.
Izi zanenedwa pa ulendo wa atolankhani omwe unakonzedwa ndi Bungwe la Malawi Economic Justice Network (MEJN)y Lachinayi pa 2 October 2025,
Ndipo a Ishmael Mussah Kaisi omwe ndi wa pampando wa Lipangala Mining Commitee yomwe ili pansi pa bungweli ati chiyambileni ntchitoyi pali mavuto ochuluka omwe anthu akukumana nawo. Ena mwaiwo ndi kusiyira sukulu panjila, kuonongeka kwa chilengedwe, kubuka kwa matenda osiyana-siyana mwa zina.
A kaisi anati ngati komiti akuyesesa kuphunzitsa anthu koma ambiri mwaiwo amaona kuti akuwaphera ufulu ochita zinthu,ndipo ambiri sakuzindikila zotsatilapo zomwe zimabwera chifukwa chokumba miyala ya mtengo wapatali motsatsata ndondomeko.
Ndipo ati pakufunika kuti mabungwe komanso boma alowelelepo kuti ntchitoyi iyende bwino.
Mayi Fainess Peter ndi mmodzi mwa alimi mderali, ndipo ati pakadali pano anasiya kulima chifukwa madzi a munsinje omwe amadalira pothilira mbewu, akumabwera ndi matope komanso mankhwala omwe akumaumitsa mbewu zawo ndipo ati njala akhalapo chifukwa amadalira nsinjewu pa ulimi wawo.
Polankhula ndi oyang’anila ntchito ku bungwe la MEJN a Cycilia Phiri ati ngati bungwe ayesesabe kugwira ntchito limodzi ndi anthu kuderali kuti miyoyo yawo ikhale yosinthika. Ndipo pasakhale
kusiyana kwakukulu pakati pa anthu osauka ndi olemela, ndichifukwa chake tikuyesesa kuphunzitsa makomiti omwe tili nawo kuti aphunzitse anthu akuderali kukhala ndi liwu pa zinthu zomwe zikuwakhuza”
Bungwe la MEJN likugwira ntchitoyi kuzera mu project yomwe ikuonenetsa kuti pasakhala kusiyana kwa kapezedwe kachuma pakati pa olemela ndi osauka ndi thandizo la ndalama kuchokera ku Norwygian Church Aid komanso Dun Church Aid .