Bungwe la National Aids Commission NAC lapempha abambo kuyika chidwi potenga nawo mbali polimbana ndi matenda a Edzi kudzera kuyezesa magazi
Nkulu wa bungweli Beatrice Matanje anayankhula izi lachiwiri kwa ntagaluka pa sukulu ya St Augustine 2 T/A Chowe mboma la Mangochi pa mwambo okumbukira matenda a edzi
Mawu ake iye anati ngakhale chiwerengero cha anthu opedzeka ndi Hiv chachepa pa zaka 15 zapitazo kuchoka pa 14 kufika pa 7 mwa anthu 100 aliwonse, ndikofunika kuti abambo achilimike podziwa mene nthupi mwawo mulili kuti akwaniritse masomphenya othana ndi matenda a Edzi.





Mlendo wolemekezeka pa mwambowu wachiwiri kwa mayor wa mangochi municipality Ishmael Woyera Nedi anathilira ndemanga ponena kuti, sionse omwe amatenga matenda kudzera mukugonana choncho, ndikofunika kuti tizidziwe mmatupi mwathu mene mulili.
Chaka chilichonse tsiku lokumbukira matenda a Edzi pa dziko lonse ndi pa 1 December ndipo mutu wa chaka chino ndi woti: Tonse Pamodzi titengepo mbali popititsa patsogolo ntchito yolimbana ndi HIV.