SALIMA ATUMIKIRABE FCB
Timu ya mpira wa miyendo ya FCB Nyasa Big , yalengeza kuti Chikumbutso Salima akhala akutumikira ku timuyi mpaka m’chaka cha 2028.
Mwambo wa gwirizanowu unachitikira ku club house ya timuyi mu nzinda wa Blantyre pa 19 June 2025.
Salima ali ndi zaka 23,
Polankhula naye, Salima wati ndi okondwa kwambiri kuti wasainiranso ku timuyi ndipo apitilidza pomwe adasiyira chifukwa ndi timu yokhayo ingapititse patsogolo luso lake.