
Apolisi ku Mangochi akusunga mchitolokosi shoveli wina wa minbus kaamba kogunda ndikupha ophunzira wapasukulu yaukachenjede ya DMI wazaka 22 usiku wadzulo lolemba pa 7 April.
Malinga ndi ofalitsa nkhani zapolisi m’bomali Inspector Amina Tepan Daudi wauza Umoyo Fm Community Radio Online kuti ophunzirayu ndi Samuel Josephy (malemu) yemwe amachokera m’mudzi mwa Chimbiya mfumu yaikulu Tambala m’boma la Dedza ndipo anali muchaka chachiwiri chamaphunziro ake.
A Daudi ati shoveliyu yemwe dzina lake ndi Mike Justine azaka 40 ochokera m’mudzi wa Mulandani mfumu yaikulu Mpama m’boma la Chiradzulu, lolemba usiku amayendetsa minibus yamtundu wa Toyota Hiace yomwe nambala yake ndi PE 10498 kuchokera ku Blantyre kupita ku Mangochi ndipo akuyandikira kufika pa Trading Centre ya DMI anakanika kuimitsa galimotolo kaamba kothamanga kwambiri zomwe zinapangitsa kuomba ophunzirayu yemwe panthawiyi amaoloka msewu ndipo a Justine ataona izi anasiya galimotolo mkuthawa.
Ndipo zotsatira zapachipatala Cha Mangochi boma zinaonetsa kuti malemuwa amwalira kaamba kuvulala kwambiri m’mutu komanso kuthyoka kwanthiti zomwe zinapangitsa kumwalilira munjira.
A Daudi ati pakati pausiku a Justine anakazipereka okha kupolisi ndipo pakalipano akuyembekezeleka kukaonekera kubwalo lamilandu.
Apolisi m’bomali akupempha anthu ogwiritsa ntchito msewu kutsatira malamulo kuti apewe ngozi zoterezi.
#LiwuLaUmoyoKwaliyense
08/04/25