Mtsogoleri wakale wadziko lino Professor Arthur Peter Mutharika yemwenso ndi mtsogoleri wachipani chotsutsa cha Democratic Progressive (DPP) lero akhala nawo pamwambo wamaliro amwana wa Mai Esther Mmadi omwe ndi mchemwali wa mai afuko akale adziko lino Professor Gertrude Mutharika.
Mwana wa mai Mmadi (McFriday) yemwe amaphunzira pasukulu ya Maranatha Boys Academy mumzinda wa Blantyre, wamwalira limodzi ndi anthu ena awiri lachiwiri usiku kumayambiriro kwasabata ino atachita ngozi galimoto zitaombana mumsewu wa John Chilembwe Highway pafupi ndi mudzi wa Mpotola m’boma la Chiradzulu.
Mwambo wamaliro ukuyembezeleka kuyamba 12 koloko masana uno ndipo uchitikira m’mudzi mwa Khwisa m’boma la Balaka.