Home Uncategorized MTSOGOLERI WAKALE WADZIKO LINO WALENGEZA KUTI AKHALA NAWO PAMWAMBO WAMALIRO MASANA ANO KU BALAKA

MTSOGOLERI WAKALE WADZIKO LINO WALENGEZA KUTI AKHALA NAWO PAMWAMBO WAMALIRO MASANA ANO KU BALAKA

by Mclove Mafuta
0 comments

Mtsogoleri wakale wadziko lino Professor Arthur Peter Mutharika yemwenso ndi mtsogoleri wachipani chotsutsa cha Democratic Progressive (DPP) lero akhala nawo pamwambo wamaliro amwana wa Mai Esther Mmadi omwe ndi mchemwali wa mai afuko akale adziko lino Professor Gertrude Mutharika.

Mwana wa mai Mmadi (McFriday) yemwe amaphunzira pasukulu ya Maranatha Boys Academy mumzinda wa Blantyre, wamwalira limodzi ndi anthu ena awiri lachiwiri usiku kumayambiriro kwasabata ino atachita ngozi galimoto zitaombana mumsewu wa John Chilembwe Highway pafupi ndi mudzi wa Mpotola m’boma la Chiradzulu.

Mwambo wamaliro ukuyembezeleka kuyamba 12 koloko masana uno ndipo uchitikira m’mudzi mwa Khwisa m’boma la Balaka.

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00