

Mlembi wamkulu ku unduna oona zaubale wamaiko akunja (Foreign Affairs) wati ndiokhutira ndimaphunziro anthumwi zamaiko am’chigawo chakum’mwera kwa Africa (SADC) aukadaulo wamakono oyang’anira chisankho chomwe chichitike maiko am’derali.
Dr Mwayiwawo Polepole auza izi Umoyo Radio Online potha pamaphunziro omwe atha lero pa 2 May omwe anayambira pa 28 April pamalo ogona alendo a Capital Hotel mumzinda wa Lilongwe.
M’mawu ake a Terry Rose omwe ndi mkulu oona zandale ku SADC ati mnthumwi zadziko la Malawi zomwe zikhale zikuyang’anira zisankho zamaiko ena monga Zambia,Tanzania ndi Seychelles zapeza ukadaulo okwana obweretsa anthu osiyana pamodzi.
Maphunzirowa mnthumwi zoposa 100 zochokera kuboma,mabungwe oima paokha komanso oimilira zipani ndiomwe anatenga nawo gawo pamaphunziropa
Wolemba : Diffrey Jonathan Bwanaisa – Mangochi
02/05/25
1 comment
Nice peace