
Mkulu wa bungwe la Malawi Electoral Commission MEC, a Justice Anabel Mtalimanja akuti kuponya voti Ku Mpata Ku Machinjiri mumzinda wa Blantyre kupitilira mpaka kufika 8 kolok usiku m’malowa.
Izi zili chomwechi kamba ka zovuta zomwe zinachita kum’mawa walero pamene anthu amayamba kuponya voti zinapezeka kuti balot paper imaoneka ngati yochongedwa kale zomwe zinapangitsa chipwilikiti pamalowa.Koma pofufunza ati panali chabe madzi amene anagwelapo.
Ndipo Izi zinapangitsa kuti anthu ayambe kuponya voti mochedwelako patadutsa maola anayi.A wapandowu anenaso kuti anthu 486 omwe maina awo anasowa kaundula boma la thyolo tsopano akwanitsa kuponya voti pamene bungweli linaonjezela nthawi paka 6 koloko.
A Mtalimanja akuyankhula izi pamsonkhano watolankhani omwe uli mkati pakalipano ku BICC mumzinda wa Lilongwe.