KHONSOLO YA MANGOCHI LILINAWO PANDANDANDA OLANDIRA NAWO GALIMOTO ZOMWE ZITHANDIZIRE KUFALITSA MAUTHENGA OKHUDZA UCHEMBERE WABWINO.

Pofuna kupititsa patsogolo ntchito yolimbikitsa komanso kufalitsa uthenga okhudza uchembere wabwino, boma la Mangochi ndi maboma ena 9 posachedwapa akhale akulandira galimoto kuchokera Ku unduna wazaumoyo.

Galimoto 16 ndi zomwe zaperekedwa Ku undunawu kuchokera ku dziko la Germany kudzera ku banki ya KFW ndi cholinga chofuna kuthandizira ntchito yofalitsa mauthenga okhudza nkhani zauchembele yomwe ilipansi pa project yotchedwa Nzatonse.

Pothilirapo ndemanga pazathandizoli, mlembi wamkulu ku undunawu a Beston Chisamile ayamikila dziko la Germany ponena kuti lafika munthawi yake potengera zoti azitha kukafika ndi mauthenga angakhale m’madera omwe amavuta kufikirika kaamba kamayendedwe.

M’mawu ake kazembe wadziko la Germany kuno Ku Malawi a Ute Konig ati dziko lawo lapereka thandizoli pofuna kufikira mwachangu ndi zipangizo zaumoyo maka kwatsikana achichepere omwe chiwelengero chotenga pakati chikumka nakwela nthawi ndi nthawi Kuti asakhale pachiopsezo.

Galimotozi zaperekedwa ku bungwe la PSI komwe iwo akapereke kumakhonsolo omwe akupindula ndi Project ya Nzatonse yomwe ikugwiridwa m’maboma a Mangochi, Mzimba, Rumphi, Ntchisi, Lilongwe, Ntcheu, Neno, Blantyre, Nsanje ndi Thyolo.

Related posts

MYSTERY DRONE BREACHES VP’s HOME.

NJOBVU YOLUSA YAPHA MLIMI WINA KU MANGOCHI.

A MUTHARIKA APEMPHA MGWIRIZANO PAKATI PAMAIKO AMU SADC KUTI NTCHITO ZACHITUKUKO ZIPITE PATSOGOLO.