
Gulu la Mangochi Makanjira road concerned citizens lapeleka masiku khumi ndi awiri ku boma kuti lifotokoze momwe likuyendetsera dongosolo lomanga msewuwo ponena kuti kupanda kutero awona chomwe angachite.
Polankhula zitantha ziwonetsero zomwe gululi linakonza lachiwiri town ya ‘bomali Patrick wasi yemwe anayankhula mmalo mwa gululi ,anati akufuna boma liwauze mmene liyendetsere dondosolo lokonza msewu wa makanjira ponena kuti ndalama zokonzela msewuwo zinabwela kale pamene tsogoleri wa dziko lino , mfumu yaikulu Makanjira ndi Phungu wa derali anapita dziko la saudi arabia kukasaina kuvomelezedwa kwa ndalama zokonzera msewuwo.
Wasi anati akufuna boma liyambe ntchito yomanga msewu wa makanjira ponena kuti anthu akukumana ndi mavuto ambiri okhuza mayendedwe.
”Zoonadi Msewu wa Makanjira Mangochi tikusindika ifeyo kuti ndalama zake tikudziwa kuti zilipo kale ,a president anatenga a MP aku Makanjira ,akhasala ndiposo a mfumu kupita ku saud arabia zokhuza za Msewu umenewu imeneyo inali mu november 2023 ,ndalamazo a saudi nde poti tikudziwa kuti ndalamazo zilipo tikudziwa pali a kuwait apelekanso ndalama komanso boma la Malawi lapelekanso ndalama nde chifukwa cha zimenezo msewu WA Makanjira ndalama zilipo kale ”Wasi anatero.
Mzika zokhuzidwa ndi kuchedwa kwa M’msewu wa Mangochi Makanjira zakhala zikupempha boma kuti lifulumizitse ntchito yomanga msewuwo pamene mbuyomu anali ndi zokambilana ndi nduna yoona za mtengatenga Jacob hara.