DZIKO LA MALAWI LIKUYEMBEKEZELEKA KUCHITITSA MSONKHANO WAZAMALIMIDWE WA MAIKO AMUNO MU AFRICA

Unduna wazamalimidwe walengeza kuti uchititsa msonkhano wachisanu ndi chiwiri (7) wasabata yapadera wamaiko amuno mu Africa(Africa-wide Agricultural Extension Week-AAEW) mwezi wamawa.

Nduna ku undunawu a Sam Kawale ati msonkhanowu uchitika kuyambira pa 12 mpaka pa 16 May pa Bingu International Convention Centre (BICC) mumzinda wa Lilongwe.

Msonkhanowu omwe uchitike mogwirizana ndi bungwe la Malawi Forum for Agricultural Advisory Services (AFAAS), at uthandizira kwambiri pobweretsa ukadaulo omwe uchokere kumnthumwi zosiyanasiyana zomwe zifike kumwambowu pansi pamutu oti “kukweza ndi kutukula ntchito zamalonda komanso mafakitale kudzera muzokolora”.

Poyankhula ndi Umoyo Radio Online a Kawale ati mutuwu omwe ulinso mmasomphenya a 2063 otukulira dziko lino uperekanso ukadaulo wina wamakono kudzera mungodya zomwe akambirane.

Related posts

https://umoyofm.mw/tigwirizane-polimbana-ndi-hiv/

TIGWIRIZANE POLIMBANA NDI HIV

ANTHU APEMPHEDWA KUSINTHA KAGANIZIDWE PA ZAMATENDA OSAPATSIRANA.