
Bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la MEC lati lichitsa kauniuni wa anthu omwe ali mundandanda ozavota kuyambira lachiwiri sabata yamawa.
Bungweli lalengeza izi lachitatu pa 7 May kudzera muchikalata chomwe latulutsa .
Kudzera muchikalatachi bungweli lati kauniuniyu yemwe cholinga chake ndikufuna kuchepetsa mavuto omwe amadza ngati anthu sanatsatire bwino ndondomekoyi pamene akudzaponya voti yawo.
Pakalipano kauniuniyu yemwe akuyembekezeleka kuti achitike m’magawo atatu, kuyambira pa 13 mpaka 15 May, 2025 afikira makhonsolo amaboma a Chitipa, Karonga, Tauni ya Karonga, Mzinda wa Mzuzu, Nkhotakota, Ntchisi, Salima, Dedza, Machinga, Chiradzulu, Neno, Phalombe, Balaka ndi Mulanje.
Gawo lachiwiri lomwe liyambe pa 21 mpaka 23 May,2025 afikira makhonsolo a Nkhata Bay, Rumphi, Likoma, Kasungu, tauni ya Kasungu, Dowa, Mchinji, Ntcheu, Zomba, Mzinda wa Zomba, Blantyre, Mzinda wa Blantyre, Thyolo ndi Luchenza.
Pamene gawo lotsiridza lidzayamba pa 29 mpaka pa 31 May,2025 m’makhonsolo a Mzimba, Lilongwe, Mzinda wa Lilongwe, Mangochi, tauni ya Mangochi, Mwanza, Chikwawa ndi Nsanje.