BUNGWE LA ESCOM LATHANDIZA AMAYI OPOSA 100 KUMAPHUNZIRO AUKADAULO WALUSO LAMANJA.

Bungwe lopelekera magetsi la ESCOM Limited, lati ophunzira achizimayi okwana 120 ndiomwe pakalipano la wathandiza kumaphunziro aukadaulo waluso lamanja ngati mbali imodzi yofuna kulimbikitsa kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna komanso amayi pantchito.

Yemwe akugwilizira ngati mneneri kubungweli a Peter Kanjere anena izi lero pa stadium ya Balaka pamwambo okumbukira tsiku la anthu ogwira ntchito omwe dziko limakhala nalo chaka ndi chaka.

Poyankhula ndi Umoyo Radio Online pambuyo polongosolera mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCathy Chakwera zina mwantchito zomwe bungwe lawo limachita, a Kanjere ati bungwe lawo lili ndi ndondomeko zokwanira zoteteza ogwira ntchito awo maka kunkhani yowateteza kunkhanza komanso kuwalimbikitsa amayi kugwira ntchito gawo lililonse powakweza m’maudindo osiyanasiyana.

Dziko la Malawi limakumbulira anthu ogwira ntchito pa 1 May, ndipo mwambo wachaka chino umakumbukilidwa pamutu oti “Ufulu kwaonse ogwira ntchito mozipereka”.

Related posts

https://umoyofm.mw/tigwirizane-polimbana-ndi-hiv/

TIGWIRIZANE POLIMBANA NDI HIV

ANTHU APEMPHEDWA KUSINTHA KAGANIZIDWE PA ZAMATENDA OSAPATSIRANA.