BOMA LAPEREKA NDALAMA ZOPOSERA K7 MILLION KUTI ZITHANDIZIRE MWAMBO WAMALIRO KWA MZIKA ZOMWE ZINAFA PANGOZI YA BUS.

Mtsogoleri wadziko lino Professor Arthur Peter Mutharika wapereka ndalama zokwana K500,000 kwa mawanja 15 omwe achibale awo anafa pangozi ya bus ku Zimbabwe paulendo wawo obwelera kuno kumudzi, kuti ithandizire pamwambo wamaliro.

Wachiwiri kwa mlembi wamkulu kuboma a Stuart Ligomeka anena izi pambuyo pamwambo olandira matupi a anthuwa omwe unachitika usiku wa lolemba pa bwalo la Kamuzu mumzinda wa Blantyre.

M’mawu awo iwo ati a Mutharika ndiokhudzidwa kwambiri ndi imfayi yomwe inachitika kumayambiliro kwa mwezi uno pa 5, ndipo ati ngati dziko lataya mzika zofunika zomwe zikanathandizira dziko lino kutukuka mmagawo osiyanasiyana.

A Ligomeka athokozanso boma la Zimbabwe pantchito yomwe yagwira pothandizira kuti matupiwa afike mdziko muno.

Matupiwa akuyembekezereka kulowa mmanda lero lachiwiri m’madera osiyanasiyana.

Related posts

MCP TO HOLD A PRESS BRIEFING AIMED TO SHARPENING THE PARTY’S FUTURE.

MKULU WINA WAPHA BAMBO AKE KAAMBA KAMPUNGA.

ANA AWIRI AFA ATAGUNDIDWA NDI GALIMOTO KU MANGOCHI.