

Banja lina lili m’manja mwa apolisi ku Chiponde m’boma la Mangochi atalipeza ndi mfuti yamtundu wa Pistol yopanda chilolezo.
Malingana ndi mneneri wapolisi m’bomali Inspector Amina Tepan Daudi wati banjali, a Sakina Mustapha ndi a Shukuran Maxon onse azaka 21, awanjata lachinayi pa 17 July pamsika wa Chiponde.
A Daudi ati patsikuli banjali linaba zovala pakaunjika wina pamsikawu, ndipo anthu omwe anaona izi anakwanitsa kugwira mayiyu ndikukampereka ku polisi komwe anapeza mfuti mchikwana chomwe anabisamo zovalazo pofuna kupeza umboni m’menemuu mkuti amuna awo atathawa.
Atafunsidwa zamfutiyo anati ndiyamunawo ndipo mosachedwa apolisi anakagwira bamboyo kunyumba kwake komwe anaulura kuti mfutiyo anaitenga mdziko la South Africa.
Pakalipano banjali likuyembekeza kukaonekera kubwalo la milandu kaamba kopezeka ndi mfuti yopanda chilolezo pambuyo pachipikisheni chomwe apolisi akuchiganizira kuti awiriwa amafuna achitire chiwembu ndi mfutiyo.A Mustapha amachokera m’mudzi mwa Mbalame pomwe a Maxon amachokera m’mudzi mwa Kajeko, mfumu yaikulu Jalasi m’boma lomweli la Mangochi.