
Bungwe la Center for Social Concerns (CfSC) lawalimbikitsa atolankhani a boma la Mangochi kuti azilemba nkhani zomwe zingabweretse ntendere pakati pa anthu pamene dziko lino likuyembezereka kuchititsa chisankho pa 16 September 2025.
Modzi mwa akulu akulu aku woyang’anira ntchito ku bungweli a Tobias Jere ndi amene wa yakhura izi pa maphunziro a masiku awiri atolankhani a bomali omwe adachitikira pa Holiday Hotel .
A Jere Analangiza atolankhani kuti apewe kulemba nkhani zomwe zingabweletse mpungwe-pungwe ndi mikangano pakati pa a Malawi. komanso kuonetsa mbali polemba nkhani zawo chifukwa zimatha kuwononga tsogolo lawo la utolankhani.
Aisha Silver mmodzi mwa a tolankhani yemwe anali nawo pa maphunzirowa wati maphunzirowa ndi ofunikira kwambiri kwa atolankhani a bomali chifukwa zawalimbikitsa kuti kalembedwe ndi kagwiridwe ntchito kawo kakhale ka ukadawulo popeleka uthenga kwa anthu moyenelera.
Dziko la Malawi likuyembezereka kuchititsa chisankho chosakha mtsogoleri wa dziko, aphungu a ku nyumba ya malamulo komanso ma Khansala pa chisankho chomwe chichitike pa 16 September 2025.