Home Uncategorized ANTHU OCHULUKA ATHA OSAVOTA NAWO NGAKHALE ALI MKAUNDULA – CSEIF.

ANTHU OCHULUKA ATHA OSAVOTA NAWO NGAKHALE ALI MKAUNDULA – CSEIF.

by Mclove Mafuta
0 comments

Anthu pafupifupi 50,000 ali pachiopsezo choti atha osaponya nawo voti mwezi wa seputembala ngati lamulo silisintha.

Wapampando wabungwe la Civil Society Elections Integrity Forum (CSEIF) a Benedicto Kondowe anena izi lero pamsonkhano omwe anakonzera atolankhani mumzinda wa Lilongwe.

A Kondowe ati malinga ndi lamulo lomwe MEC linakhadzikitsa loti anthu adzaponya voti yawo komwe analembetsera kuphinja anthu ambiri kuphatikizirapo asilikali omwe azikapereka chitetezo kumalo oti sanalembetsereko.

Kudzera mukalata lomwe alembera mtsogoleri wadziko lino yomwenso ayipereka kwa sipikala wanyumba yamalamulo, amabungwe komanso zipani zandale, apemphamo mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCathy Chakwera kuti kudzera kumphamvu zomwe anapatsidwa ayitanitse msonkhano wa aphungu a nyumba yamalamulo kuti akaunikire ndikusintha lamuloli lomwe lilimugawo 74 loyendetsera malamulo adziko lino ndicholinga chofuna kuonetsetsa kuti aliyense yemwe alimkaundula odzaponya voti athe kutero kulikonse komwe akukagwira ntchito panthawiyi.

A Kondowe atinso izi zipereka mwai wapadera kwa omwe akukagwira ntchito zosiyanasiyana patsiku lovotali kuti akaponye nawo voti kudzera mundondomeko yomwe ayipemphayi kotero kuitanitsa mkumanowu kukufunika machawi nyumbayi isanatsekedwe.

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00