


Anthu okhala ku Mangochi awapempha kuti achotse kaganizidwe kolakwika komwe kamadza pamene munthu wamwalira mwadzidzi.
Pempholi ladza potsatira kafukufuku watsopano yemwe wonetsa kuti anthu pafupipafupi 40 pa anthu 100 aliwonse akumamwalira pachaka kaamba kakusowekera kwa mauthenga okhudza matenda osapatsirana monga kuthamanga kwa magazi, mtima, shuga, mphumu, khansa, kusokonekera kwa ubongo komanso matenda akugwa, mwaena, zomwe ati anthu ena amapezerapo mpata omanyoza amzawo kuti ndi mfiti.
Mkulu oona zamapulani ndi chitukuko kukhonsolo yabomali a Chris Nawata omwenso anaimilira komiti yaikulu yabomali (District Executive Committee-DEC) ndiomwe anapereka pempholi pomwe avomereza bungwe la Adventist Development and Relief Agency (ADRA) Malawi kubweretsa project yomwe cholinga chake ndukufuna kupereka uthenga omemeza anthu kudziwa zambiri zokhudza kupewa ndi kupeza chithandizo panthawi yomwe azindikira kuti ndiokhudzidwa ndi matenda osapatsiranawa.
A Nawata ayamikira bungwe la ADRA poganizira boma la Mangochi ndi projectiyi zomwe ati ithandizira kutseka mauna omwe analipo osowekera mauthenga okhudza matendawa.
Poyankhula ndi wailesi ya Umoyo Fm wapampando ogwilizira bungwe la ADRA Malawi mdziko muno Dr Martha Kamwiyo ati ali ndi chikhulupiliro kuti projectiyi ibala zipatso zabwino pounikira kuti agwira ntchito ndi m’nthambi zonse zoyenera kuphatikizirapo komiti zakumidzi zomwe zikafikitse uthenga kwa anthu oyeneranso.
Dr Kamwiyo ati akonzanso dongosolo lomwe aphunzitse aphunzitsi okwana 450 kuchokera msukulu zokwana 100 zaboma kuphatikizapo zomwe sizaboma komanso kufalitsa uthenga kudzera kuwailesi zakumidzi ndicholinga choti uthenga okhudza kupewa, kusamala komanso kupeza thandizo okhudza matenda osapatsiranawa ufalikire paliponse.
Bungwe la ADRA Malawi ndithandizo lochokera kubungwe la UNICEF lasonkhanitsa ndalama zokwana K35million zomwe zigwire ntchito m’madera amafumu andodo atatu monga Namkumba,Mponda ndi Chimwala kuyambira mwezi wa November chaka chino mpaka mwezi wa January chaka chamawa.