


Namatetule pandale mai Patricia Kaliati apempha amai omwe akupikisana mipando yosiyanasiyana pachisankho chapa 16 September kuti alunjike pamfundo zawo zachitukuko panthawi yomwe akuchititsa misonkhano yawo yokopa anthu.
A Kaliati omwe anali mlendo olemekezeka apereka pempholi ku Mangochi, pamkumano omwe unakonzedwa ndi bungwe lolimbikitsa amai kupikisana nawo pa ndale la Centre of Civic Society Strengthening.
Iwo ati kudzikweza panthawi yomwe akuchita misonkhano yawo kutha kuchepetsa mwai wawo opambana kotero nthawi isanathe akuyenera kukhala odekha ndipo atambasule zitukuko zomwe azawachitire anthu akudera kwawo.
“Sichinthu chabwino kuima pamsonkhano mkumalengeza kuti ife ndi owinawina!uko amayi amzanga dziwani kuti ndikulakwitsa chifukwa voti ya munthu imafunika kunyengelera polunjika pazomwe iye akufuna”. Anatero a Kaliati.
Potsiridza a Kaliati amemanso amayiwa kuti achilimike kunyengo zomwe angakumane nazo monga kulandira zitonzo zosiyanasiyana kuchokera kwa abambo omwe akupikisana nawo zomwe zingawafooketse kuti asiyire panjira ndipo atsindika ponena kuti nthawi yakwana yoti amai ochuluka alowe m’bwalo.
Pothilirapo ndemanga a Flora Habibu Paseli, oima paokha omwe akupikisana nawo pa mpando wa ukhansala mu ward ya Majuni m’boma la Mangochi, ati aphunzira zambiri kudzera kumkumanowu monga kulimba mtima, posaziyang’anira pansi kuphatikizirapo ukadaulo wamene angakopele anthu kuti awavotere.
A Paseli atinso maphunzirowa mwazina awasintha kaganizidwe kochita ndale zawo monyoza ena kuti akondedwe koma kutsamira mfundo zomwe zingathetse mavuto lomwe dera lawo lilinawo mothandizidwa ndi khonsolo, anthu akufuna kwabwino, abwenzi komanso thandizo la mipingo logwira ntchito zachifundo.