Pulezidenti wadziko lino Professor Arthur Peter Mutharika yemwenso ndi mtsogoleri wamaiko am’chigawo chakum’mwera Kwa Africa (SADC) maka kumnthambi yoona zachitetezo ndi ubale, wapempha maikowa kubwera pamodzi ndi kuchilimika pofuna kupititsa patsogolo ntchito zachitukuko.
A Mutharika anena izi Ku Lilongwe pamkumano wamaikowa omwe unachitikira kunyumba yachifumu ya Kamuzu Palace lachisanu komwe anakumananso ndi atsogoleri akale monga Dr Joyce Banda komanso a Jakaya Kikwete omwe analamulirapo dziko la Tanzania.
Atsogoleri akalewa motsogozedwa ndi a Kikwete, anatsikimizira a Mutharika kuti ntchito yolimbikitsa mtendere wamaiko amu SADC pakali pano ikuyenda bwino maka mmaiko a Democratic Republic of Congo (DRC), Lesotho, Madagascar ndi Mozambique.
Atsogoleriwa ndiomwe akutsogolera komiti ya SADC ya anthu achikulire pomwe a Jakaya Kikwete alikhala pampando pamene Dr Banda ndiomwe ali wachiwiri wawo.