World Cup Qualifiers 2026
Timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino ya Flames yafananidza mphamvu 2 kwa 2 ndi timu ya Liberia mu mpikisano odzigulira malo mu chikho cha World Cup Qualifiers 2026.
Masewerowa anachitikira pa bwalo la masewero la Bingu National Stadium mu nzinda wa Lilongwe.
Timu ya Liberia ndi imene idayamba kumwetsa chingoli mu chigawo choyamba patadutsa mphindi zitatu pomwe chigoli cha chiwiri chinafika patadutsa mphindi 61 mchigawo cha chiwiri kudzera mwa nyamata wawo Ayouba Kosiah.
Timu ya Flames idazambatu mu gawo la chiwiri pamene Gabadinho Mhango ndi yemwe adagolotsa chigoli choyamba ku timuyi patadutsa mphindi 71 pomwe Chawanangwa Kaonga anamwetsa chigoli cha chiwiri cha timu ya Flames.
Ndipo Mphunzitsi Wa timu ya Flames a Kalisto Pasuwa adayamikira anyamata ake kuti adasewera bwino ngakhale kuti sadapambana masewerowa pamene Mphunzitsi yu akukonzabe timuyi.
Pasuwa adatinso vuto lomwe wawona ku timu yake ndi kukanika kudula mipira (side piece) komabe ayetsetsa kukonza vutoli.
M’mene zatelemu timu ya Flames ili ndi mwayi ochepa opitilira kukamenya nawo mu chikho cha World Cup, pomwe timu ya Tunisia yazigulira kale malo ku world cup ili nambala yoyamba ndi Ma points 13 mu gulu H.