
A Malawi okwana 41 pa 100 alionse ati ali ndi malingaliro odzavotera a Peter Mutharika a chipani cha Democratic Progressive (DPP), pomwe anthu 31 pa 100 aliwonse akuti adzasankha mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress (MCP) a Lazarus Chakwera ndipo ena 6 pa 100 alionse asankha a Dalitso Kabambe a chipani cha UTM.
Izi ndi malingana ndi kafukufuku wa bungwe la Institute of Public Opinion and Research omwe waonetsanso kuti anthu atatu pa 100 asankha kudzavotera a Atupele Muluzi achipani cha United Democratic Front (UDF) ndipo awiri asankha a Joyce Banda.
Bungweli latsindika kuti izi sizikulosera mmene zidzakhalire pa chisankho cha chaka chino, koma zikungoonetsera m’mene anthu akufunira pakadali pano, ndipo lapempha mbali zosiyanasiyana kugwirana manja polimbikitsa anthu kuti adzatuluke kukavota.