
Bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lalengeza kuti lidzawerengera mavoti pamanja osati pamakina .
Mai Justice Annabel Mtalimanja omwe ndi wapampando wabungweli, anena izi lero ku Lilongwe, pamwambo otsegulira nyengo yochititsa misonkhano yokopa anthu pachisankho chapa 16 September.
A Mtalimanja ati ntchito yowerengera mavotiyi idzayambira kumalo komwe kwaponyedwa voti kuyambira omwe akupikisana pa mpando wa utsogoleri,aphungu ndi kumalizira makhansala ndipo zonse zidzachitika poyera.
M’mawu awo atatsegulira kampeniyi iwo apempha atsogoleri azipani kuchita misonkhano yawo yokopa anthu mwabata ndi mtendere, posanyadzitsa azipani zina ndipo m’malo make alunjike pamfundo zachitukuko zomwe azikomza zomwe adzachite akapambana.
Bungwe la MEC lati kampeniyi ichitika kwa miyezi iwiri (masiku 60) kuyambira pa 14 July mpaka pa 14 September ndipo lachenjeza kwa onse omwe adzachite misonkhano yawo mosemphana ndi nyengoyi lamulo lidzagwira ntchito.