
Bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la MEC lalengeza kuti lolemba pa 14 July, lichititsa mwambo waukulu okhadzikitsa masiku amisonkhano yomwe cholinga chake ndikukopa anthu maka kwa omwe akudzapikisana pachisankho chapa 16 September.
Malinga ndi chikalata chomwe wasayinira mkulu ofalitsa nkhani ku bungweli a Sangwani Mwafulirwa, ati mwambowu omwe uchitikire ku BICC mumzinda wa Lilongwe, akawukhadzikitsa pamutu oti “kulimbikitsa utsogoleri wabwino kudzera muvoti yanu” ubweretsa pamodzi mnthumwi zazipani 24 zomwe zalembetsa, atsogoleri omwe apikisane pampando waupulezidenti omwe ndioima paokha, mnthumwi zaboma,nyumba zoulutsira mawu komanso mabungwe osiyanasiyana.
A Mwafulirwa atinso ku mwambowu bungwe la MEC likatsikimizira anthuwa mene lakonzekelera chisankho kuti chikhale chabata, mtendere komanso chokomera aliyense kudzera mundondomeko zake zomwe linadzikhadzikitsa.