
Mawanja omwe anavutika ndi ng’amba okwana 13,997 okhala m’madera a Makanjira ndi Lulanga ku Mangochi, akuyembekezeleka kulandira thandizo la chimanga ndi mnthambi yoona zangozi zogwa mwadzidzidzi ya DoDMA kuyambira lero.
Potsindikizira URS Online zadongosololi mneneri ku khonsolo ya Mangochi Bishop Witmos wati matumba achimanga okwana 13,313 adzera panyanja ya Malawi kuchokera ku Monkey-Bay pasitima ndipo matumba 684 adzera nawo pamsewu ndi galimoto la bungwe loona zachakudya padziko lonse (World Food Program -WFP).