NDIKUFUNA NDISINTHE KAONEKEDWE KA MANGOCHI MUNICIPAL
Rodrick Clement Chiwaya yemwe akupikitsana nawo pa mpando wa phungu Mangochi Municipal chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) wati ndi khumbo lake kuti asinthe kaonekedwe ka Mangochi.
Kuzela mu nsokhano omwe anachititsa lachiwiri 10 Seputembala pa bwalo lochitilapo nsonkhano mu ward ya Kalungu, Chiwaya anati ndiokhumudwa ndi mmene town imaonekera maka tikamalowa m’bomali chifukwa alendo amalandilidwa ndi zinyalala zimene zili zolakwika mu boma lomwe limalandila alendo tsiku ndi tsiku.
Chiwaya anatinso nthawi ya mvura anthu amavutika mayendedwe kamba ka madzi ndipo wati azaonetsetsa kuti wakonza ngalande zonse za mmisewu ya tawuniyi.
Polankhula ndi khansala wa Kalungu Kenneth Chimombo anati anthu aku kalungu amusankhebe chifukwa anatha kukwanilitsa zitukuko zimene anthu aku wardiyi anamupempha monga kuika mipope, kukonzanso misewu komanso kulipilira ana sukulu ndipo ana okwana 16 ndipo omwe anapindula.
Chiwaya akuchititsa misonkhano yokopa anthu mma ward onse omwe ali mu Constituency ya Mangochi Municipal mosogozedwa ndi makhansala onse.
78
previous post