Timu ya FCB Nyasa Big Bullets mogwirizana ndi banki ya FCB akonza Chikondwelero choti bankiyi yakwanitsa zaka makumi atatu(30).Ndipo mwambowu uchitike Lamulungu pa 29 June 2025 mu nzinda wa Lilongwe pa Bingu National Stadium.
Pa tsikuli kudzakhalanso masewero a mpira wamiyendo apakati pa FCB Nyasa Big Bullets yomwe izakumane ndi timu ya Silver Strikers.
Malinga ndi mmodzi mwa akulu akulu a timu ya FCB Nyasa Big Bullets a Albert Chigoga ati mwambowu ukuchitika ngati mbali imodzi yolemekeza bank ya FCB imene akhala nayo pa ubale kuyambira m’chaka cha 2023.
Masewerowa akuyembekezereka kuzayamba nthawi ya 3 koloko masana, ndipo cholinga cha masewerowa ndikufuna kupeza ndalama zomwe akufuna kugura zipangizo zogwiritsira ntchito ana omwe akusulidwa pa luso la mpira ku Luwinga Inclusive Academy mu nzinda wa Mzuzu.
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets idangonjesapo timu ya Silver Strikers mu chikho cha TNM Super League mwezi wa April ndi chigoli chimodzi kwa Duu, komanso ma timu awiliwa akuyembekezereka kukumana pa 12 July chaka chino mu ndime yotsiliza ya Airtel Top 8.