FDH Bank Cup iyamba pa 5 july2025
Mayere a chikho cha FDH Bank anachitika Lachiwiri pa 24 June, 2025 ku chiwembe Ndipo masewero oyambirira mu ndime yachipulura azaseweredwa pa 5 July komaso pa 29 July.
Ndipo Bank ya FDH yati yawonjezera thandizo la ndalama zomwe zimapelekedwa ku masewero a mpira wa miyendo dziko muno mu chikho cha FDH Bank Cup kuchoka pa K150 Million kufika pa K250 Million, izi ndi malingana ndi oyang’anira za malonda ku bankyi a Ronald Chimchere.
Ndipo iye anaonjezera kunena kuti “kukhazikitsa kwa chikho cha FDH Bank Cup ndi kofunika kwambiri chifukwa zipititsa patsogolo masewero a mpira wa miyendo dziko muno”.
Katswiri wa chikhochi chaka chino azalandira ndalama zokwana, 45 million kwacha ndipo timu yachiwiri izaladira ndalama zokwana 20 million kwacha.
Matimu 16 a mu Tnm Super League, 12 omwe akusewera mu NBS Bank National Division komanso 51 kuchokera mzigawo zonse zinayi za dziko muno ndi omwe akhale akulimbirana ukatswiri wa chikhochi chaka Chino.