YEMWE AKUDZAPIKISANA NAWO PAMPANDO WAPHUNGU M’DERA LA MANGOCHI MUNICIPAL WAYAMBA NTCHITO YOMANGA ZIPATALA ZING’ONOZING’ONO

Pofuna kuchepetsa kuthinana kwa anthu ofuna thandizo pachipatala chachikulu chaboma la Mangochi,a Idi Kalosi omwe akudzapikisana nawo pampando waphungu m’dera la Mangochi Municipal alonjeza zomanga zipatala zing’onozing’ono kuti athane ndi vutoli.

‎‎A Kalosi omwe akuimira chipani cha United Democratic Front (UDF) anena izi lero pambuyo poyendera ntchito yomanga chipatala kwa Mosiya yomwe ilimkati pakalipano.‎‎Poyankhula kugulu la anthu lomwe linasonkhana m’derali, iwo ati anaona kuti ndichanzeru kuyambiratu kumanga chipatalachi pofuna kuwatsikimizira anthu kuti ndiokonzeka kuwatumikira angakhale chisankho sichinaponyedwe.‎‎

Potsindika iwo ati nkhani za umoyo atsogoleri ochuluka amaziyang’anira pansi kwambiri chonsecho ndigwero  lazonse kotero ati asunga ndalama zankhaninkhani zomwe zigwire ntchito pomanga zipatalazi m’madera ozungulira dera la  Mangochi Municipal kuti atukule ku ntchito zaumoyo.‎‎

Ndipo pomaliza apempha anthu kuti adzawavotere ngati akufuna kudzalandira zitukuko zomwe derali likusowekera monga kukonzanso misewu yomwe imavuta kudutsika mu nthawi yadzinja, kuphunzitsa achinyamata ntchito zamanja komanso kupereka mwai wangongole kwa amayi kuti azichitira bizinesi zosiyanasiyana.

Related posts

ANTHU APEMPHEDWA KUSINTHA KAGANIZIDWE PA ZAMATENDA OSAPATSIRANA.

ENA MWA MAUDINDO A BOMA AYIMITSIDWA

TIKUYEMBEKEZERA MASEWELO APAMWAMBA