Bambo wina wazaka 31 ku Mangochi ali m’manja mwapolisi kaamba kopezeka ndimakala opanda chilolezo.
Malinga ndi mneneri wapolisi m’bomali Inspector Amina Tepan Daudi wati bamboyu yemwe dzina lake ndi Mark Yusuf ochokera m’mudzi mwa Chomba mfumu yaikulu Mponda m’boma lomweli la Mangochi anamunjata kum’mawa kwa lachitatu pa 30 April ntownship yabomali atatsinidwa khutu kuti mkuluyo akutsitsa matumba ankhaninkhani kunyumba kwake.
Poyankhula ndi Umoyo Radio Online a Daudi ati iwo limodzi ndi ofesi yoyang’anira nkhalango m’bomali atakachita chipikisheni kunyumbayo anakwanitsa kupeza matumba amakala okwana 212 komanso zipika zamitengo zokwana 27.
Yusuf akuyembekezeleka kukayankha mlandu ogwiritsa ntchito nkhalango opanda chilolezo.