MZIKA ZAPEMPHEDWA KUSANKHA ATSOGOLERI AMASOMPHENYA.

Gulu lomwe silandale la Mkamulano wa Yao ku Mangochi, lapempha anthu okhala m’bomali kuti azasankhe phungu yemwe ali ndi mfundo zachitukuko.

Wachiwiri kwa wapampando wa gululi a Kida Adams anena izi lachinayi pa 17 July, pamkumano omwe linakonza ndi anthu omwe akudzapikisana pampando waphungu a mdera la Mangochi Municipall.

Polankhula ndi URS, a Adams ati anthu okhala m’derali akuyenela kusankha phungu ochokera mdera lomweli kaamba kakuti ndi amene angadziwe bwino mavuto omwe anthu amakumana nawo nthawi ndi nthawi.

Iwo apemphanso anthu kuti apewe kusokoneza misonkhano ya ndale poyambitsa zipolowe koma agwiritse ntchito mwaiwu kuti adzikamva mfundo zothyakuka kuchokera kwa anthuwa kuti adzasankhe phungu oyenera.

Pothilirapo ndemanga a Idi Carlos omwe alinawo mundandanda odzapikisana nawo m’dera la Mangochi Municipal ngati phungu wachipani cha United Democratic Front (UDF), ayamikira gululi kaamba kokonza mkumanowu omwe ati ndi opindulitsa kumbali yoonetsetsa kuti anthu akudera akulandira zitukuko zomwe akusowekera.

Gulu la Mkamulano wa Yao linakhazikitsidwa ndi cholinga chofuna kulankhulira anthu omwe amakhala m’boma la Mangochi pa mavuto osiyanasiyana omwe anthu a m’bomali amakumana nawo.

Related posts

https://umoyofm.mw/tigwirizane-polimbana-ndi-hiv/

TIGWIRIZANE POLIMBANA NDI HIV

ANTHU APEMPHEDWA KUSINTHA KAGANIZIDWE PA ZAMATENDA OSAPATSIRANA.