CHIWELENGERO CHA ANTHU OFUNA KUDZAIMIRA PA MPANDO WA PULEZIDENTI NDIPO ALIPIRA SOPANO CHAKWANA 10

Bungwe la Malawi Electoral Commission MEC lati chiwelengero cha anthu amene alipilira K10,000 ndikutenga kalata zawo zofuna kudzaimila pa udindo wa tsogoleri wa dziko lino tsopano chafika pa 14 .

Malingana ndi Bungwe la MEC,chiwelengerochi chafika pa 14 pamene a David Mbewe a chipani cha Liberation for Economic Freedom Party (LEFP) atenga kalata zawo ku bungweli.

Mwa anthu 14 omwe atenga kalata zawo ndi kulipila kubungweli kuti azapikisane pa mpando wa tsogoleri wa dziko,4 ndi woima paokha.

Zipani 24 ndi zomwe zidalembetsa m’kaundula wa zipani m’dziko lino ndipo pakadali pano zatsonyeza kuti zipani 10 ndizomwe zatsala kukatenga kalata zawo zofuna kuzapikizana nawo pa chisankho cha pa 16 september 2025.

Bungwe la MEC likulimbikitsa anthu omwe akufuna kudzaimila nawo mmaudindo osiyanasiyana komanso zipani kuti akalipire nthawi yolipira ndikutenga kalata zawo isanathe.

Related posts

ANTHU APEMPHEDWA KUSINTHA KAGANIZIDWE PA ZAMATENDA OSAPATSIRANA.

ENA MWA MAUDINDO A BOMA AYIMITSIDWA

TIKUYEMBEKEZERA MASEWELO APAMWAMBA