Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCathy Chakwera wayamikira bank ya Reserve (RBM) kaamba kochilimika pochepetsa mavuto akusowa kwa ndalama zakunja.
Dr Chakwera ayankhula izi lero ku Lilongwe pamwambo okumbukira kuti bankiyi yatha zaka makumi asanu ndi limodzi (60) ikugwira ntchito zake, poonetsetsa kuti chuma chadziko lino chikuyenda bwino.
Iwo ayamikiranso bankiyi kaamba koika ndondomeko zina zamakono loti dziko lino lidzipata phindu lochuluka kudzera muntchito zake.
M’mawu awo Dr McDonald Mafuta Mwale omwe ndi mkulu wanankiyi, ati pofuna kuthana ndimavuto azachuma omwe dziko lino limakumana nawo, pakufunika kuchilimika maka pomatumiza ndikugulitsa katundu wapamwamba m’maiko akunja.